Boma likuyembekezeka kugawa masikito mdziko muno

Advertisement
John Bande

Boma lati ligawa masikito otetezera ku udzudzu mzigawo zonse m’dziko muno pofuna kuthana ndi nthenda ya malungo yomwe ikadaperekabe chiwopsezo chachikulu pa umoyo ndipo ntchitoyi igwilika ndi thandizo la ndalama pafupifupi 84 biliyoni kwacha lomwe ipeleke ndi bungwe la Global fund.

Malingana ndi m’modzi mwa akuluakulu ku nthambi ya unduna wa za umoyo mdziko muno, a John Sande, dziko lino likuyembekezeka kulandira ndalama zokwana USD82 million kuchokera ku Global Fund zothandizira pa za umoyo ndipo ndalama zokwana USD50 million ndizomwe zidzagwire ntchito yogulira komanso kugawa masikitowa.

A Sande anapitiliza kufotokoza kuti ntchito yakalembera wa anthu omwe atapindure nawo  idzayamba m’mwezi wa September ndipo kugawa kudzachitika m’mwezi wa November  kumapeto a chaka chino.

A Sande amayankhula izi ku Blantyre ku msonkhano wa atolankhani omwe unakonzedwa ndi a MOMENTUM TIYENI ndipo iwo anafotokozanso kuti kalemberayu achitika kudzera pa kompyuta pofuna kupewa mavuto ena omwe analipo mbuyomu.

Wolemba: Ben Bongololo