Wadzetsa chisoni Kondwani: amusumira Kachamba Ngwira

Advertisement

…150 miliyoni ya anthu inasokonekera
…musamvere zachambazo – akutero Kachamba Ngwira

Inu amene mumaziona mutatsegula kampani zanu za sopo, kaya kupanga shuga, enanu ma juwisi ndi zimzake, iwalani zimenezo. Mkulu analonjeza zokhutitsa a Malawi ndi luso la mu mafakitale, a Kondwani Kachamba Ngwira, awatengera ku bwalo. Ati adyera anthu ochuluka amene ankakhulupilira malonjezo awo aja.

Malinga ndi Malipoti amene a Malawi24 taona, anthu okwana 40 amene anadedeluka ndi kutengeka ndi malonjezo a Kachamba akalira ku bwalo kuti mkukuyi adawayenda njomba. Maripotiwa aonetsa kuti Kachamba Ngwira sakufotokoza zogwira mtima pa ndalama yokwana 150 miliyoni Malawi Kwacha.

Maripoti ena amene atsindikizidwa akuonetsa kuti Kachamba amauza anthu kuti asonkhe ndalama zoti atsegulire kampani. Anthu anasonkha kuti ayambitse malo omwetserapo mafuta, minda ikuluikulu komanso kampani zina zosangalatsa mmaso. Koma ati kufika lero palibe kalikonse.

Ati anthu akapereka ndalama zawo, Kachamba amawayika mu gulu la pa WhatsApp. Chodabwitsa ndi choti anthu amene anadabwa ndi malonjezo a mkuluyu ndipo amafunsa mafunso kuti zili pati, iye amawathotha mu gulumo.

Mmodzi mwa anthu amene anathamangitsidwa mu gulumo ndi kudyeredwa ndalama zake wadandaula kuti Kachamba akuchita u khuluku.

“Chimene amachita ndi choti amakamba nkhani zake zija zosintha dziko, ine ndinaperekako ndalama kuti ndilowe mu gulu. Koma mpaka pano palibe chimene chimaoneka, amangokamba nkhani basi. Pofunsa kuti ziri pati, ndinangoona wandichotsa,” anatero munthuyu.

Kachamba ati waberanso ena powanamiza kuti awaphunzitsa luso. Mmodzi mwa oberedwa ndi phungu wa ku nyumba ya malamulo amene anamupatsa Kachamba Ngwira 400 sauzande Malawi kwacha kuti azaphunzitse anthu a mu dera lake luso lopanga zinthu.

“Analandira ndalama koma kenako anayamba kuzembazemba. Mpaka pano sanabwere,” wadandaulidwa motero Kachamba.

Mwini wake nkhani Kachamba Ngwira wati anthu akumuyipitsira mbiri chifukwa cha majelasi. Ati zoti wabera anthu ndi nkhani za chamba basi zomwe akutsogolera ndi a ndale ena chifukwa akuchita nsanje ndi chikoka chake.

Advertisement