Ndikawina konveshoni ya DPP ndipo ndizakhala mtsogoleri wa Malawi — Nankhumwa

Advertisement

Mtsogoleri wa zipani zotsutsa kunyumba ya malamulo a Kondwani Nankhumwa wati kuyambira 2025, iye ndi amene akhale akutsogolera dziko la Malawi.

Polankhula ndi a Brian Banda, a Nankhumwa ati iwo atenga chipani cha DPP kuchokera kwa a Peter Mutharika.

“Konveshoni ya chaka chino ya DPP, ine ndikawina ndipo ndikatenga u President wa chipani chimenechi,” anatero a Nankhumwa motsindika. Pofunsidwa kuti chikuwalimbitsa mtima ndi chani, iwo anati akudalira Yesu.

Atafunsidwa a Nankhumwa ngati iwo akuziona ali mtsogoleri wa dziko kudzera mu chipani cha DPP, iwo ananena kuti akuziona zitatero.

“Anthu pano akufuna DPP ndipo ine ndikulowa m’boma ndi chipani chimenechi,” iwo anatero.

Atafunsidwa kachikena ngati iwo azakhale mtsogoleri wa Malawi, a Nankhumwa anakhala ngati achita njengunje ndi kudzati iwo akhala mtsogoleri ngati Mulungu angafune.

A Nankhumwa koma anatsindika kuti ali ndi kuthekera konse kokhala mtsogoleri wabwino kuposa a Chakwera amene akutsogolera pano.

“Ine ndakhala mu boma, ma unduna osiyanasiyana ndipo ndikudziwa chochita,” anatero.

Pa nkhani yokhudzana ndi ubale wawo ndi a Mutharika, iwo anatsindika kuti ubale wawo ulibwino ndipo amasokoneza ndi anthu a dera.

“Ine ndi a Mutharika sitinasinthanepo Chichewa, ndi anthu ena chabe kupanga ndale,” iwo anatero.

Follow us on Twitter: