
Chiwerengero cha anthu amene akutsikira kuli chete kamba ka ngozi zogwa mwa dzidzi chikunkira chikwerelakwelerabe m’dziko muno.
Nthambi ya boma yoona za ngozi zogwa mwadzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (DODMA) yati mwezi wa January chiwerengerochi chakwera kufikira pa anthu 31 amene amwalira ndi ngozizi kuchokera pa anthu 11 amene anamwalira m’mwenzi wa December chaka chatha.
Mneneri wa nthambiyi, Chipiliro Khamula wati anthu okwana 22 ataya miyoyo yawo kamba mphenzi zomwe zimagwa m’dera osiyanasiyana dziko lino mu nyengo ino ya mvura.
Khamula anapitiliza kufotokoza kuti pafupipafupi anthu okwana 31, 413 akhudziwa ndi ngozizi kuyerezeka ndi mwezi wa December chaka chatha pamene 10, 833 ndi amene anakhudzidwa ndi vutoli.
Boma kudzera mu nthambiyi, likuchenjeza anthu mdziko muno kuti akhale osamala popewa ma ulendo pamene mvura ya ziphaliwali yayamba.