
Moto olusa wawotcha sitolo ndi kupha anthu awiri a banja limodzi komanso kutentha ma sitololo oyandikirana nawo kwa Chemusa mu nzinda wa Blantyre lero.
Malinga ndi mtsogoleri wa mu msikawu, a Hastings Kabango, banja lomwe lakumana ndi tsokali ndi la a Masina omwe amachita malonda ogulitsa zipangizo zosiyanasiyana (hardware).
Apolisi atsimikiza za ngoziyi ndipo ati motowu unayamba chifukwa cha mbaula yomwe inagwila mafuta otchedwa finasi omwe anakuza mphamvu ya moto.
A Barnet Msonyo omwe anawona ngoziyi ikuchitika ati pa nthawi ya ngoziyo banja la aMasina linali likukonza chakudya cha masana ndipo moto unagwira Finasi zomwe zinapangitsa sitolo yawo iyake moto wamphamvu mpaka anakanika kutuluka ndipo anafera momwemo.
A Kabango anati mu sitolomu mudalinso mwana wa malemuwa yemwe anthu anakwanitsa kumupulumutsa.
Finasi ndi mafuta a mphamvu omwe sachedwa kugwira moto ngati momwe amakhalira mafuta a nyale ndi a galimoto ndipo amagwiritsidwa ntchito posungunula zinthu monga paint, kupaka matabwa kuti chiswe chisadye ndinso kuthamangitsira chiswe kumene.
Sorry for that.may their souls rests in peace.let us all pray for this.