Inu mumatonza boma la Tonse kuti linanama pa lonjezo lawo la ntchito 1 miliyoni, gwetsani nkhope yanu mwamanyazi. Inu mukudikila kuti mupezepo pa ntchito zija, kwezani chikhulupililo chifukwa zayamba kutheka.
Amene anali mkulu wa bungwe lothana ndi katangale la Anti-Corruption Bureau a Reyneck Matemba apatsidwa ma udindo ena awiri mu boma atakana kuti apitilize ngati mkulu wa bungwe lothana ndi katangale.
A Matemba amene boma la Tonse linawapempha kuti apitilize ntchito yawo yothana ndi katangale ngakhala kuti kontarakiti yawo inatha, anakana ntchitoyi mu sabatayi ndi kupempha boma kuti lipeze munthu wina apitilize ntchitoyi.
Koma boma la Tonse lawakamila a Matemba ndipo lawapatsa ma udindo ena awiri atsopano.
Malinga ndi malipoti otsimikizika, a Matemba tsopano ndi mlembi wamkulu mu unduna wa zachilungamo komanso akhala mkulu oona zolemba malamulo mu boma ndi kukambilana ma kontarakiti a boma, solicitor general pa chingelezi.
Koma a Matemba anena kuti kutula pansi udindo ngati mkulu wa ACB achita kumapeto kwa January kuno kupangila kuti obwela mmalo mwawo azapeze pofikila.
A Matemba anasankhidwa pa udindowu ndi mtsogoleri opuma a Peter Mutharika. Ma lipoti ena osatsimikizika akusonyeza kuti boma likulingalila zotenga mayi Martha Chizuma kuti atenge udindo wa a Matemba.