Zionetsero zomwe mzika zokhudzidwa ku Mulanje zinakonza kuti zichitike la Chiwiri likudzali pa 17 Novembela zalepheleka.
Malinga ndi wapampando wagululi a Oliver Andrys ati ganizoli ladza ponena kuti agwilitsa ntchito njira yokambirana potula madandaulo awo ku boma.
Wapampandoyu wati ganizoli ladza kutsatira pambuyo pa zokambirana ndi anthu onse okhudzidwa m’bomali.
Iye anati anthu onse okhudzidwa agwilizana kuti zionetserozi zisachitike pambuyo powunikira bwino kuti anthu ena amapezerapo mwayi osokoneza mabizinesi, kuba katundu komanso kuyambitsa ziwawa.
Apa bwanamkubwa wabomali a Chriss Nawata ati alirandira bwino ganizoli ndikunena kuti mzika zikuyenera kuti zizigwilitsa ntchito njira yokambirana ndipo zionetsero zizikhala kuti njira zonse zavuta.
Mzikazi zinakonza zionetserozi pa kusakondwa ndi vuto la kusowa kwamafuta ndi kuzimazima kwa magetsi.