Ntchito yoyima ku mizere yosaka Mafuta, ganyu osaka ndalama zakunja mwa mavuto ena zipitilira kwa miyezi ina khumi pomwe Boma lakana msatsi ponena kuti mavutowa adasiya ndi a Boma lomwe lapita la Malawi Congress ndipo zufunika nthawi.
Nduna yofalitsa nkhani a Shadric Namalomba awuza nyumba ina yofalitsa nkhani kuti pakufunika zaka ziwiri kuti ndondomeko zomwe Boma la a Mutharika linayika ziyambe kugwira ntchito.
A Namalomba poyankhapo pa mfundo zomwe andale ena akuti Boma lalephera kukonza chuma cha dziko lino iwo ati Boma lawo langotha chaka ndi miyezi isanu ndi iwiri ndipo pakufunika nthawi kuti zinthu zisinthe.
M’modzi mwa akatswiri pa ndale a James Hiwa ati kulozana zala mkosayenera pa nthawi ino yomwe mavuto akuta dziko lino.
A Hiwa ati aMalawi atopa ndi kudzisasa kwa adindo kuti mavutowa si iwo apangitsa pomwe aMalawi akupitirirabe kuvutika.
“Nduwona ngati kukanirana ukuku mkosathandiza aMalawi, aliyense akudziwa kuti Boma la MCP lidasokoneza zinthu ndipo boma lapano liyang’ane njira osati kuloza MCP” Anatero a Hiwa.
A Hiwa ati Boma likonze chuma ndi kusintha zinthu zomwe zikuwasautsa aMalawi pano.
Posachedwapa mtsogoleri wa chipani cha United Transformation Movement UTM Dalitso Kabambe akhala akutsindika kuti Boma la a Mutharika likukanika kukonza chuma cha dziko lino zinthu zomwe zikuwayika aMalawi pa moto wa lawi-lawi.








