Adindo m’boma la Kasungu awapempha kuti awonetsetse kuti zitukuko zonse za pansi pa thumba lakudera, Reformed Constituency Development Fund (RCDF) zisachitike mwakaphulira, ponena kuti ndalama za a Malawi zikuyenera kugwira ntchito bwino.
Phungu wadera la Kasungu Manisipalite, Noel Mkubwi wati zidzakhala zoipa kuti pomwe boma likupereka ndalama za chitukuko zochuluka kulipira ma kontilakitala kenako chitukukocho chaweyeseke munthawi yochepa.
Mkubwi wayankhula izi sabata ino pa mwambo wokhazikitsa ntchito za chitukuko pansi pa thumba la RCDF pa mwambo omwe unachitikira pasukulu ya pulayimale ya Mtsita mdera la mfumu yayikulu Kaomba m’boma la Kasungu.
Phunguyu wapempha adindo osiyanasiyana kuti agwirane manja ponena kuti ndalama zomwe zikugwira ntchito m’thumbali ndi misonkho ya aMalawi omwe amadulidwa misonkho kuti chitukuko chimenechi chiyende bwino.

“Ena alibe silipasi, alibe sapato koma akadulidwa msonkho zikulowa m’thumba limeneli kuti zipindulire kutukula madera athu,” watero Mkubwi.
Mkubwi wati adindo atengepo mbali komanso kuwonetsetsa kuti palibe nkhani za katangale, ziphuphu komanso kuwonetsetsano kuti zitukukozi zikhale zolimba makamaka kwa makontrakita.
Yemwe anayimira makontirakita pa mwambowu a Mordecai Chilopola wa kampani ya Emmanuel General Construction wati nawo mafumu ndi akomiti apewe kugwiritsa ntchito mphamvu pa momwe makontirakitawa angalembere anthu ogwira ntchito.
A Chilopola anati izi zimachititsa kuti anthu omwe alibe ukadaulo ndiwo apeze ntchito zomwe mapeto ake ntchitoyo sikhala yolongosoka.
Poyankhulapo, mkulu wa khonsolo ya Kasungu Manisipalite a Wanyapakucha Mzumara wati, pakadali pano boma lidapereka kale ndalama zokwana 20 za omwe akumanga zitukuko za CDF.
Malinga ndi a Mzumala cholinga cha boma poperekelatu ndalamazi ndikufuna kuwonetsetsa kuti pasakhale kuchedwa kwa ntchitozi.
Naye khansala wadera la Chimphangwe Witness Mtanga, yemwe ntchito yomanga zipinda zophunziliramo yayamba kale mdera lake wati akuyembekezera chitukuko cholimba chomwe chidzakhalapo mpaka nthawi yayitali.





