Pomwe mpikisano uliwonse umayenera kupindulira kampani komaso makasitomala, zikuwoneka kuti mpikisano wa Coca-Cola ukupindulira mbali imodzi yokha pomwe makasitomala ambiri ati akukaikira ngati anthu akupambanadi mphoto.
Kampani ya Coca-Cola inakhazikitsa mpikisano mwezi wapitawo, omwe uli mkati pano ndipo ukupereka mpata kwa anthu mwayi opambana mphoto yomwe yalembedwa mkati mwachitsekerero cha botolo la chakumwa chawo.
Izi zapangitsa anthu kumagula zakumwa za kampaniyi kwambiri ndi ganizo loti atha kupata mphoto zosiyanasiyana monga filiji, mayikolowevu ndi zina, koma zikuwoneka kuti anthuwa akungomwa osapambanako.
Kudzera pa funso lomwe tinafusa pa tsamba lathu la fesibuku Lachinayi m’mawa, zadziwika kuti anthu alibe chikhulupiriro ngatidi pali anthu omwe apambanako mphoto mumpikisanowu.
Mai wina yemwe akugwiritsa ntchito dzina loti Chi Pie analemba kuti “Mpaka crate kutha, zingotidwalitsa sugar🤣,” kuphera mphongo pa chikaiko chomwe ambiri ali nacho pa mpikisanowu. Nawo a Veronica Mnalemba sanafune kupsatira mawu: “Gas atipweteka eeh.”
Kaamba ka mkwiyo, ena afika potchula mpikisanowu kuti ndiwabodza; a John Kachulu ati “aaah ndizabodza izizi angofuna atimwetse zawozi pa ulele.” Nawo a Zangazanga Junior Blessings angoyankhula chindunji; “kulibe anawinapo.”
Ena mwa anthu omwe ayika ndemanga apempha bungwe lomwe limayang’anira mipikisano ngati iyi m’dziko muno kuti lichitepo kanthu popanga kafukufuku ngati mpikisanowu uli weniweni.
Chikhazikitsidwireni mpikisanowu, kampani ya Coca-cola siinabwerepo poyera ndikuulutsa mayina a anthu omwe achita mphumi mumpikisanowu.
