Ndithu nyengodi ikusintha, nanga June apezeka bwanji m’mwezi wa Malitchi. Awa ndimafunso omwe aMalawi ena akudzifunsa kamba koti m’madera ena mdziko muno akulandira mvula ya mphamvu, ena yowaza. Nde nkumati kodi chimanga sichionongeka chili m’munda pamene anthu akuyembeza kuti chiume ndikukolora?
M’madera a ku m’mwera nyengo yakhala ili yofunda ndi ya mvula yamawawa sabata ino ndipo Nthambi yoona za nyengo mdziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati nyengo ya mitambo ikuyembekezereka kupitilira m’madera ambiri mdziko muno ndipo kumwera mvula idzigwa yamawawa pomwe kumpoto mvula idzigwa yamabingu ndi yamphamvu nthawi zina.
“Tiyembekezere nyengo yamitambo komanso ya chifunga ndi mvula yomwe idzigwa yamphamvu maka m’madera akumpoto. Masana a lero tiyembekezere nyengo yamitambo komanso ya mvula m’madera ochepa koma yamphanvu maka m’madera akumpoto,” yatero Nthambiyi.
Ndipo m’maiko ena, ku Ethiopia anthu okwana 30 afa pamene mvula ya mphamvu idagwa ku Gano Zone ku m’mwera kwa dzikoli. Izi zidachitikanso mdziko la Kenya masiku apitawa ndipo anthu ena adafa kamba ka mvula ya mphamvu yomwe idagwa mdzikolo. Masabata apitawo dziko la Madagascar lidatayanso nzika zake kamba ka mvula ya mphamvu yomwe idaononga miyoyo komanso katundu waanthu ambiri.








