
Timu ya Chelsea usiku uno yakodola timu ya Tottenham Spurs mu mpikisano wa English Premier League (EPL) kuti agumulane masewelo awo a chi nambala 30 pa bwalo la Stanford Bridge mu mzinda wa London.
Chelsea yomwe inapita kopumulira (International break) itagonja kangapo, sikuwawonela kukondwa ma timu a Manchester City ndi New Castle omwe ayima kutsogolo kwake, kutchingira Chelsea kuti isapeze mpata omenya nawo Champions League (UCL)
Pomwe awiriwa akulowa m’bwalo lero, usiku wapitawu Liverpool yakulitsabe chigwembe chake ndi Arsenal pomwe chigoli cha Diogo Jota chavulaza Everton 1-0 pa bwalo la Anfield kuti iyo italikire ndi ma points 12, ndipo Manchester City yalumalitsa Leicester City poyikankhilabe ku phompho ndi zigoli 2-0.
Masewelo Asanu ndi amodzi usiku wathawu ayenda motele;
⚽ Manchester City 2-0 Leicester
⚽ Liverpool 1-0 Everton
⚽ Newcastle 2-1 Brentford
⚽ Bournemouth 1-2 Ipswich
⚽ Southampton 1-1 Crystal palace
⚽Brighton 0-3 Aston Villa