Mithi wamangidwa kamba kofalitsa kuti MEC yafufuta maina a anthu ena mkaundula

Advertisement
Mzuzu Police

Nthambi ya zachitetezo ya Malawi Police Service (MPS), yati Julius Mithi wamangidwa kamba kolemba pa tsamba lake la fesibuku kuti bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lafufuta anthu okwana 1,152,091 mundandanda wa anthu omwe akuyenera kudzaponya voti pa chisankho chikubwerachi.

Mneneri wa nthambi ya MPS Peter Kalaya, wati kumangidwa kwa Mithi kukutsatira dandaulo la ma bungwe a MEC komaso NRB. Kalaya wati Mithi yemwe akusungidwa ku polisi ya Mzuzu, atengeredwa ku bwalo la milandu pasanathe maola 48 monga mwa malamulo.

Nkhaniyi ikubwera pomwe posachedwapa zinadziwika kuti mayina a m’modzi mwa ma komishonala a bungwe la MEC, Francis Kasaila pamodzi ndi mkazi wake, sakupezeka mukaundula wa anthu oti adzaponye voti.

Potsatira nkhani ya ku Dowa kwa mayina a Kasaila, anthu akhala akufalitsa mphekesera yoti mayina aanthu ochuluka akusowa mukawundula wa MEC, zomwe zinapangitsa mtsogoleri wambali yotsutsa boma kunyumba ya malamulo a George Chaponda, kupempha kuti pachitike kawuniwuni wapadera pa mndandanda wa anthu omwe akuyenera kudzavota pa 16 September, 2025.