Ulendo uno mukabera zisankho ndidzathana nanu – Mutharika

Advertisement
DPP

Mtsogoleri wakale wa dziko lino yemwenso ndi mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive (DPP), Peter Mutharika wanenetsa kuti masankho amene akubwera pa 16 September ngati patadzachitike m’chitidwe obera, iwo ndi chipani chawo sadzalora ndipo adzathana ndi oyenera kuthana nawowo.

A Mutharika ati masankho a m’chaka cha 2020 anavomeleza kulandidwa boma chifukwa sanafune za nkhondo, apo ndi pomwe ati ulendo uno sadzavomelanso kupangidwa chipongwe.

Iwo ayankhula izi pomwe anapita kukagawira chakudya kwa anthu a chipembedzo cha chisilamu m’boma la Mangochi maka mnthawi ino pomwe akusala kudya, ndipo atsindika mawu awo kuti akubwera kudzapulumutsa dziko lino tsopano pomwe likudutsa mu mnyengo zothina.

“Ulendo uno mukabera chisankho ndidzathana nanu, pa 2020 ndinavomeleza kubeledwa chifukwa sin’nafune nkhondo,” anatero a Mutharika.

Iwo adzudzulanso m’chitidwe omanga anthu a chipani chawo cha DPP, pomwe ati dziko lino ndi lawina aliyense mosayang’ana chipani kapena munthu.

Mtsogoleriyu wapemphanso asilamu kuti pamene Ali mu nyengo ya kusala kudya, apemphelelenso chisankho chomwe chikubwera pa 16 September kuti Chidzayende bwino.

A Mutharika anali ndi mayi wakale wafuko a Gertrude Mutharika ndi atsogoleri ena a chipani cha DPP.