
Anyamata anu mwawatuma ku Tunisia aja afikako koma kwatsala ndikubweletsa zotsatira tsopano.
Timu ya dziko lino yampira wamiyendo yatera mdziko la Tunisia lero kudzera pa bwalo la Ndege la Tunis-Carthage International, pomwe ikuchalira kuvungumulana ndi timu ya dzikolo Lolemba lino.
Timu ya dziko lino yomwe yanyamuka dzulo, idzikapita pa bwalo la Hammadi Agrebi ikuchokera kosakazidwa ndi Namibia 1-0, ndipo idzikakumana ndi Tunisia yomwe ili pa nambala 1, pomwe Malawi ili pa nambala 4 onse mu guru H.
Kuyambira pa mndandanda momwe akuchitira bwino, mu guru H muli ma timu a Tunisia, Namibia, Liberia, Malawi, Equatorial Guinea ndi Sao Tome and Principe.