Gangata wati alibe mantha

Advertisement
Alfred Gangata

“Kaya ndi kundipha pa zifukwa za ndale andiphe koma sinditopa,” watelo Alfred Gangata yemwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo cha pakati, pomwe amalankhula pa area 3 mu mzinda wa Lilongwe kutsatira kutulutsidwa kwawo pa belo ya bwalo yomwe oweluza milandu ku bwalo la Lilongwe awapatsa lero.

A Gangata omwe adawamanga lolemba powaganizira kuti akugwiritsa ntchito satifiketi ya folomu folo yomwe anaipeza mwa chinyengo mchaka cha 2018, ati anthu owalondalonda maka pa zifukwa za ndale sakuyenera kupanga nawo mantha chifukwa iwo ndi wachiwiri chabe kwa mtsogoleri wa chipani, ndipo ati anthu ayembekezere kuti iwo amangidwa kuposa apa.

A Gangata omwe anawelenga malemba a m’buku lopatulika kuchokera pa Eksodo 13 ndime 14 ati mavuto omwe akuwoneka pakadali pano anthu sadzawawonanso kuyambira pa 16 September 2025.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipaniyu amutulutsa pa belo pomwe oweluza milandu ku bwalo la milandu la Lilongwe magistrate Austin Banda ati ambali yaboma analephera kubweretsa umboni wogwirika kuti a Gangata angasokoneze mboni zaboma.

A Banda anatinso panalakwika kuti zikalata zowamangila a Gangata zinakatengedwa ku bwalo la milandu la ana zomwe zinali zosayenera chifukwa a Gangata simwana ndipo mlandu wawo sukukhudza ku bwalo la ana.

A Gangata agona mchitolokosi mwa apolisi masiku atatu ndipo dzulo milandu yawo inakanika kulowa ku bwalo la Lilongwe pomwe anadzapita nawo ku bwalo la Nkukula m’boma la Dowa komwe anawabwezanso kuti abwelele ku Lilongwe komwe oyimira boma pa milanduyi anapempha oweluza kuti akapeleke belo kwa aGangata ponena kuti ali ndi uthenga (intelligence) kuti a Gangata akasokoneza mboni za boma.