
Madam Speaker tsiku lina mnyumba ya malamulo muno mudzakhala chipwilikiti muno…ndukuuzani Madam Speaker..!! musandiuze kuti ndikhale chete, muno mudzabwera chipwilikiti.
Phungu wa Nyumba ya Malamulo wa Mzimba North a Yeremia Chihana ati wina asamayankhule za ku dera lawo pomwe ndalama za ku dera lawo za Constituency Development Fund (CDF) zinawonongedwa ndi khonsolo ya bomali kusamalira madongosolo a kubwera kwa mkazi wa mtsogoleri wa dziko a Monica Chakwera ku Edingeni ndipo ati ndalama zokwana 130 million Kwacha za ku madera a aphungu a m’boma la Mzimba zinawonongedwera limodzi.

Nkhaniyi inayamba pomwe phungu wa dera la Mzimba South a Emmanuel Chambulanyina Jere anati nkhani yoti khonsolo ya Mzimba inawononga ndalama kusamalira ma dongosolo a kubwera kwa mkazi wa mtsogoleri wa dziko ku Edingeni m’bomali yomwe analankhula a Chihana ndi yabodza.
A Jere anati ndalama zomwe khonsolo ya Mzimba inawononga zinabwezedwa koma a Chihana sakudziwa chifukwa samapezeka ku zokambirana za pa khonsolo poti amangokhalira kuyenda mayiko a kunja.
A Jere ati ndalama zomwe khonsolo ya Mzimba inagwiritsa ntchito sizinali za Constituency Development Fund (CDF).
A Chihana anati zakhala bwino kuti a Jere avomeleza kuti khonsolo inawononga ndalama za ku madela a aphungu zomwe mzosayenera, ndipo ati iwo anawuza unduna wa zamaboma a ng’ono kuti akufuna ndalama zawo zomwe adawawonongera, koma unduna wa zamaboma ang’ono udati m’malo mwake ungowamangira chitukuko m’malo mwa kubweza ndalama zomwe iwo anakana.
Mkulu okhazikitsa bata mnyumbamu a Jacob Hara ati iwo pokhala m’modzi wa aphungu a ku Mzimba, khonsolo ya boma lo inabweza ndalama zomwe zinagwiritsidwa ntchitozo ndipo ati ma lipoti alipo. Apo a Hara alangiza a Chihana kuti adzipezeka ku zokambirana za pa khonsolo.
Nduna ya zachuma a Simplex Chithyola Banda analowelera kunena kuti mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino amagwiritsa ntchito ndalama zomwe zimaikidwa pa dongosolo la zachuma lopita kwa mtsogoleri wa dziko ndipo sizingatheke kuti agwiritse ntchito CDF.