Kwelepeta wadandaulira boma kuti litsekule chipatala cha Domasi Community

Advertisement
Kwelepeta

Nyimbo yoti chipatala cha Domasi Community m’boma la Zomba chitsekulidwa yakhala nyimbo yomwe yalira motopetsa. Phungu wa dera la Zomba Malosa a Grace Kwelepeta omwe lero mnyumba ya malamulo apemphanso unduna wa za umoyo kuti uganizire zotsekula gawo la OPD pa chipatalachi, ngakhale mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera mwezi wa July anati analandira ma lipoti kuti zambiri pa chipatalachi zatha ndipo mbali ina ya OPD ndi yokonzeka kuyamba kugwira ntchito.

Phunguyu anayima mnyumba ya malamulo mu mzinda wa Lilongwe, kufunsa wachiwiri kwa nduna ya za umoyo a Noah Chimpeni, kuti utsekula liti chipatala cha Domasi Community ponena kuti chipatalachi nchofunika kwambiri kwa anthu okhala m’madera ozungulira.

Koma poyankha a Chimpeni sanatchule nthawi yomwe chipatalachi chingayambe kugwira ntchito ndipo anangoti zili m’malingaliro a boma kuti atsekule chipatalachi ndipo akhale akuchitsekula kuti chiyambe kugwira ntchito

Mwezi wa July 2024 mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera pomwe anakhala nawo pa mwambo opeleka sukulu za ukachenjede za Nalikule ndi Domasi m’boma la Zomba zomwe zinamangidwa ndi thandizo la boma la Japan, adati sakanayendera Nalikule ndi Domasi pomwe chipatala cha Domasi chisadamalizikitsitse.

Apo mtsogoleri wa dzikoyu anati adalandira lipoti kuti chipatala cha Domasi ndi chokonzeka kuyamba kupeleka thandizo ku mbali ya OPD ndipo adati apo mpamene amavomeleza zobwera ku Zomba.

Chipatala cha Domasi Community chinayamba kumangidwa mchaka cha 2013 ndipo chakhala chikuyenda mwa liwilo la nkhono maka kwambiri chifukwa cha kupelewera kwa ndalama zopita ku ntchitoyi, koma pakali pano gawo lalikulu la ntchitoyi linagwirilika.