Nzika iliyonse ya dziko lino ili ndi ngongole yosachepera K809,500 ku maiko akunja

Advertisement
Chithyola Banda

Nduna ya za chuma a Symplex Chithyola Banda yauza nyumba ya Malamulo kuti dziko lino pofika September, 2024 linali ndi ngongole yosachepera K16.19 trillion ku maiko a kunja.

Pa chifukwa ichi, mzika za dziko lino zomwe ndi zopyola 20 miliyoni, aliyese ali ndi udindo obweza ngongole ku maiko a kunja ndalama yoposera K809,500 kuti dziko lino lithane ndi ngongoleyi.

Izi zili chomwechi chifukwa dziko lino lakhara likubwereka ndalama ku maiko a kunja mowirizika kamba kolephera kupanga zinthu zokwanira zoti ndi kugulitsa ku maiko a kunjawa.

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus  Chakwera Lachinayi lathali anali ndi nkumano ndi achinyamata a m’chigawo cha kum’mwera ku nyumba ya chifumu ya Sanjika kumene analengeza kuti dziko lino lakhala likupanga ndondomeko ya za chuma podalira ndalama zobwereka maiko a kunja ndipo ili ndi vuto lalikulu limene likupangitsa kuti ngongoleyi ichuluke kwambiri.

Mawu ake, Banda wati ndondomeko ya chuma ch adziko lino mu chaka cha 2024-2025, ndalama zokwana K6.14 trillion ndi zomwe boma ligwiritse ntchito.