M’bindikiro pa ofesi ya DC wa boma la Balaka wayambika

Advertisement
Balaka District Council

Anthu a m’mudzi mwa Ng’onga, mfumu yaikulu Nsamala m’boma la Balaka ayamba m’bindikiro pa ofesi ya bwanamkubwa wa bomali ati pofuna kukakamiza unduna wa maboma ang’ono kuti usamutse bwanamkubwa wa bomali, Tamanya Harawa.

M’modzi mwa akuluakulu omwe akonza m’bindikiro wu, Armson Kabvalo wati akuchita izi potsatira kutha kwa masiku asanu ndi awiri omwe anapereka ku undunawu kuti ukhale utayankha za pempho lawo.

A Kabvalo ati bwanamkubwa yu sakuwathandiza pankhani yokhudza chipukuta misonzi cha malo awo omwe kampani yopanga Cement ya Portland idagula.

Ndanga
Ndanga: Sitichoka.

Anthuwa akhala akudandaula kuti kampaniyi idapeleka chipukuta misonzi chochepa kwambiri.

Alinane Ndanga, yemwe ndi wapampando wa gulu la anthu akwa Ng’onga omwe akuchita m’bindikiro pa ofesi ya bwanamkubwa wa boma la Balaka, wati iwo sachoka pa malowa kufikira atapatsidwa mayankho omveka bwino pa pempho lawo.

Ndanga wati iwo sanagulitse malo awo ku kampani ya Portland Cement ndipo m’malo mwake anangowuzidwa ndi akuluakulu ena kuchokera ku boma kuti anthuwa asamuke pamalopo chifukwa boma lili nawo ntchito malowa.

Anthuwa awopsezanso kuti achita chothekera chilichonse kuti ateteze malo a makolo awo.