
Nduna yowona za maboma ang’ono ndi chitukuko cha kumudzi, a Richard Chimwendo Banda ati ngati pali phungu wa kunyumba ya malamulo yemwe wasakaza ndalama za ku dela ndi wa Mzimba north, a Yeremia Chihana, ponena kuti wakhala akugwiritsa ntchito ndalama za Constituency Development Fund (CDF) molakwika.
Ndunayi yalankhula izi mnyumba ya malamulo lero mu nzinda wa Lilongwe, pomwe ati ali ndi ma umboni okwana kuti a Chihana sanayendetse bwino ndalama za mu thumba la CDF kudera kwawo.

Nkhaniyi inayamba pomwe a Chihana amatsilira ndemanga pa za zomwe mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera anayankhula lachisanu lathali mu State of the Nation Address-SONA yawo, ndipo a Chihana ati dziko lino ladutsa mu mphepo ndi mvula zowononga (cyclones) potchulanso kuti dziko ladutsanso mu Cyclone Chakwera.
Izi sizidakomele mtsogoleri wa zokambirana mnyumbayi Richard Chimwendo Banda, yemwe anati phungu wa Mzimba north nthawi zonse amabweretsa chisokonezo mnyumbayi.
A Banda anati kulankhula kotelo ndi kowononga, ndipo amayenera abweze mawuwo (withdraw).
Sipikala wa mnyumbayi a Catherine Gotani Hara analamula kuti a Chihana abweze mawu ndipo anabweza posinthanitsa mawuwo ndi cyclone wa boma ili.