Chakwera atule pansi udindo – Suleman

Advertisement
Sameer Suleman

Ku Nyumba ya Malamulo kudayaka moto dzulo pamene phungu wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) Sameer Suleman, adauza nyumbayi kuti mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera atule pansi udindo wake kaamba kouza aMalawi bodza panthawi yomwe amatsegulira mkumano wa nyumbayi.

Mpungwepungwe udakula mnyumbayi a Suleman atangolankhula izi, ndipo mtsogoleri wa nyumbayi Richard Chimwendo Banda anauza aphungu otsutsa kuti akapitiliza mchitidwewu awawonetsa.

Anthu ambiri mdziko muno akhala akudzudzula mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera kamba koti adafwanthamula bodza pamene amatsegulira Nyumba ya Malamulo sabata latha pa zitukuko zomwe boma lake lapanga.

Zambiri za zitukuko zomwe Chakwera anati boma lake lachita ndi kumanga nyumba za a polisi zokwana 24 m’boma la Likoma. Koma zinadziwika kuti m’bomali mulibe ngakhale nyumba imodzi yomwe inamangidwa.