![President Trump](https://malawi24.com/wp-content/uploads/2024/11/Donald-Trump-640x400.jpg)
Kwanu kwanu m’thengo mudalaka njoka. N’kutheka a malume kapena azakhali adatchona mu dziko la Amereka lija ndi kuwaona tsopano. Tsache limene anyamula bambo Trump lokonza mu dziko la Amereka likhudza mzika zina za dziko lino zimene tsopano zili pa mzere kudikila kukwera ndege kumabwelera.
Malipoti ochokera mu dziko la Amereka asonyeza kuti a Malawi okwana 56 ndiwo ali pa mndandanda wa anthu amene mtsogoleri wa tsopano wa dzikolo a Donald Trump walamura kuti azibwelera kwawo.
Malingana ndi malipotiwa, anthuwa ati ndi omwe amakhala mu dzikolo mopanda chilolezo ndipo ena anapalamulako milandu yosiyanasiyana.
Atangolumbiritsidwa bambo Trump adatenga tsache ndi kuyamba kusesa mu dziko la Amereka, kugwira anthu amene sakuyenera kukhala mu dzikolo ndi kuwabwenzera mmakwawo. Mayiko ena adakhala akunyinyirika kulandira anthu awo koma ataopsezedwa ndi bambo Trump, mayikowo avomereza.
Malinga ndi mndandanda umene Malawi24 yaona, dziko la Mexico ndilo limene liri ndi anthu ochuluka amene akhale akuonetsedwa msana wa njira. Pali mzika za dzikoli zoposera 252000 zimene zikhale zikupitikitsidwa.
Mu Africa muno, dziko la Nigeria nalo likhala likulandira mzika zochuluka. Anthu 3690 ndiwo akhale akukakamizika kubwelera kwawo.
A Donald Trump, amene anakhalakonso mtsogoleri wa dziko la Amereka, abweleranso pa mpando. Iwo analumbira pa 20 January.
Atangolumbira, bambo Trump anaiyambapo yosintha malamulo amene anakhadzikitsidwa ndi mtsogoleri wakale wa dzikoli a Joe Biden.
Pa nthawi imene amachita kampeni, a Trump adalonjeza kuti azaonetsetsa kuti anthu onse okhala mu dziko la Amereka opanda chilolezo apitikitsidwa.
bwana trump