Bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) lero latseka malo omwetsera mafuta a Ntcheu Puma Fueling Station chifukwa chophwanya malamulo a za mphamvu, pogulitsa mafuta mu zigubu ndi mu ma drum kwa mavenda.
M’modzi mwa akuluakulu a bungwe la MERA, a Vitumbiko Sakala atsimikiza za nkhaniyi ponena kuti bungwe la MERA lidatulutsa kalata kuletsa kugulitsa mafuta mu zigubu zosaloledwa koma ati pali malo ena omwetsera mafuta omwe akupitilira kuphwanya malamulo.
A Sakala alangiza eni malo omwetsera mafutawa kuti ayike ndondomeko zokhwima kuwonetsetsa kuti malo awo omwetsera mafuta akutsata ndondomeko zomwe zili mu malamulo a MERA.
A Sakala ati bungwe la MERA likhale likuyenda m’malo osiyanasiyana mdziko muno kutseka ma fueling station omwe akugulitsa mafuta mzigubu ndi cholinga choti mafuta azipezeka mdziko muno.
Izi zathera kuti anthu anayi omwe amagwira ntchito pa malo omwetsera mafuta a Ntcheu Puma ayamba awayimitsa ntchito atachita zotsutsana ndi zomwe akuluakulu anawawuza kuphatikiza kuwaletsa kugulitsa mafuta mzigubu.
Chaka chatha bungwe la MERA lidatseka malo ena atatu mu mzinda wa Lilongwe ndi maboma chifukwa chophwanya malamulo.