Phungu wa boma la Dedza cha ku m’mawa a Joshua Malango limodzi ndi aphungu a mbali ya boma m’nyumba ya malamulo agwira pakhosi phungu wa DPP a Sameer Suleman kuti awachotse pa udindo wa wapampando wa komiti ya za ulimi ya m’nyumba ya Malamulo.
A Malango omwe ndi phungu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) anayimaponso m’nyumbayi m’mwezi wa April 2024 kuti a Suleman awachotse, kachiwiri anayimanso m’nyumba ya malamulo lachinayi kupempha nyumbayi kuti awachotsenso pa mpandowu ponena kuti samaonetsa khalidwe labwino monga wa pamphando wa komiti ya za ulimi wa nyumbayi, komanso adakalankhula ndi atolankhani atatulutsidwa m’nyumbayi.
Nyumbayi inasokonekera lachinayi pamene a Malango anavumbulutsa pempho lawo aphungu aboma anagwirizana ndi a Malango, koma wachiwiri kwa sipikala wa nyumbayi a Madalitso Kazombo anati nkosayenera kukamba za munthu amene m’nyumbayi mulibe komanso a Suleman adalandira chilango chawo chowayenera.
Aphungu a mbali yabomayi ati a Sameer Suleman amapanga zosayenera pamene adapita kukayendera ofesi za bungwe la SFFRFM pomwe anali atayimitsidwa kwa masiku asanu kuti asabwere kunyumba yamalamulo.
Mtsogoleri wa aphungu otsutsa a George Chaponda ati nkhani yomwe akukakamira aphungu aboma ndi yosathandiza ndipo sikoyenera kukambilana za munthu amene palibe komanso adalangidwa kale ndi sipikala wanyumbayi
Nyumba ya Malamulo lachisanu inayimitsidwa kawiri mowirikiza pofuna kulora kukambilana zina mwa zofunika pa zokambirana za aphungu kuphatikiza nkhani yokhudza a Suleman ndipo zokambilana za akuluakulu oyendetsa zokambirana (business committee) adzapitiliza kukambilana zokambiranazi lolemba.
M’mwezi wa April a Malango atapempha za kuchotsedwa kwa a Malango, sipikala wa nyumbayi a Catherine Gotani Hara adauza a Malango kuti atsate ndondomeko zoyenera pobweletsa pempho lawoli.