Unduna wa za maphunziro wati pakutha pa zaka zitatu zomwe zikubwerazi ukufuna kufikira ophunzira a msukulu zonse za m’dziko muno ndi thandizo la chakudya kudzera mu ndondomeko yopereka chakudya kwa ophunzira ya chaka chino mpaka chaka cha 2030 yomwe ayikhazikitsa.
Mlembi wamkulu mu undunawu a Mangani Chilala Katundu ndiye wanena izi lachinayi mu m’zinda wa Lilongwe pomwe undunawu, mogwilizana ndi mabungwe ena okhudzidwa, amakhazikitsa ndondomekoyi.
Malingana ndi a Katundu, ngakhale ndondomekoyi ndi ya chaka cha 2030, palikuthekera kuti ikwanilitsa zolinga zake chisanafike chakachi ponena kuti magulu okhudzidwawa ndiwodzipereka kwambiri pofuna kuwonesetsa kuti ophunzira onse akupeza thandizoli.
Ndipo kumbali yake, mkulu wa bungwe la Mary’s Meals kuno ku Malawi Angela Chipeta Khonje wati padakali pano bungweli lakwanitsa kufikira ophunzira 1.1 Million sukulu za mmaboma 24 a mdziko muno ndipo pano likufuna kufikira ena pafupifupi 300,000 zaka zikubwerazi.
Koma poyankhulapo pa zakukhazikitsidwa kwa ndondomekoyi,
mkulu wa bungwe la National Planning Commission (NPC) Dr. Thomas Munthali wati akukhulupilira kuti ndondomekoyi ithandiza kwambiri kuti dziko lino likwanitse masomphenya ake a chaka cha 2063.