Lolemba lokha palibe alepheletse ziwonetsero, wanenetsa Namiwa

Advertisement
Namiwa

Silvester Namiwa yemwe ndi mkulu wa bungwe la Center for Democracy and Development Initiative (CDEDI), wabetchera kuti kubwele mvula ngakhale kuwombe dzuwa, ziwonetselo za Lolemba sizilepheletsedwaso ndi akuluakulu a boma monga zachitikila za lero.

Akulu akulu a boma, alepheletsa ziwonetselo zomwe bungwe la CDEDI linakonza zofuna kukakamiza mkulu wa bungwe la MERA Henry Kachaje komanso nduna ya za mphamvu Ibrahim Matola kutula pansi udindo polephera kuthetsa vuto la kusowa kwa mafuta a galimoto.

Kudzera mu kalata watulutsa bwanankubwa wa boma la Lilongwe Lawford Palani, kulepheletsedwaku kukutsatila mkumano wambali zokhudzidwa Lachitatu. Iye wati patsikuli apolisi akhala otangwanika, choncho m’malo mwake zionetserozi zichitike lolemba pa 25 November 2024.

Poyankhapo za kusinthidwa kwa tsikuli, Namiwa wati: “Ulendo uno okha sitilolaso zoti wina atilepheletse kuchita zionetsero chifukwa ndi ufulu wathu. Tikukamatcha ku Capital hill mpaka mkulu wa MERA, Henry Kachaje komanso nduna yowona zamphamvu Ibrahim Matola atule pansi udindo chifukwa alephela kuthana ndi vuto lakusowa kwamafuta.”

Iye wati aMalawi ambiri ndiokhumudwa kuti boma silikuwonetsa chidwi chenicheni chofuna kuthana ndi vuto lakusowa kwa mafuta a galimoto zomwe wati zakhudza ntchito za malonda.

Advertisement