Pali chiopsezo chakubuka kwa nthenda ya kolera ku dera la Mpamba

Advertisement
Nkhatabay

Anthu oposera 2000 a m’mudzi mwa nyakwawa Kamphalo m’dera la Mfumu ya ikulu Timbiri ku Mpamba m’boma la Nkhata-Bay ali pa chiopsezo chotenga matenda a kolera kamba kakusowa kwa madzi a ukhondo kuderali.

A Dorothy Chirwa awuza Malawi24 itayendera derali kuti madzi ndi ovuta kwambiri ndipo amamwa madzi amuzithapwi.

“Kuno kwathu madzi ndi wovuta kwambiri, timamwa madzi amuzithaphwi ndipo nthawi zambiri timatsegula m’mimba, kunena zowona vuto ili ndilalikulu, ndipo sitikuziwa kuti tilowera kuti panopa,” anatero mai Chirwa.

Mkulu wa bungwe la Community Development Footprints (CDF) a Charles Chingwalu omwe bungwe lawo likugwira zintchito zosiyanasiyana kuphatikizapo za umoyo ndi maphunziro kuderali, ati anthu adera la Kamphalo akusoweka madzi a ukhondo.

“Takhala tikugwira ntchito kuderali kwa zaka ziwiri tsopano ndipo mavuto omwe akuta derali ndi ambiri, ndipo vuto lomwe likufunika kuthetsa mwachangu ndi la madzi, anthu kuno kulibe madzi a pa mjigo kapena m’mipopi ndipo anthu amagwiritsira ntchito madzi amuzithaphwi. Tikupempha adindo athandize anthuwa kupewa matenda akolera,” iwo anatero.

Boma la Nkhata-Bay linali boma limodzi lomwe linakhudzidwa kwambiri ndi matenda a kolera mzaka za mbuyomu.

Advertisement