Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera watsimikizira bungwe la International Monetary Fund (IMF) ndi World Bank kuti dziko la Malawi lipitiliza kuika njira zabwino zokwezera chuma chake.
Chakwera wanena izi pa mkumano ndi akuluakulu a ma bungwe awiriwa, Kristalina Georgieva wa IMF komanso Anna Bjerde wa Banki yaikulu pa dziko lonse mu mzinda wa Washington DC mdziko la United States of America.
“Panali kufunika kuti mtsogoleri wa dziko lino akumane ndi atsogoleri a mabanki awiriwa kuti awatsimikizire za kudzipereka kwawo pakusintha chuma cha dziko la Malawi kuti mzika zake zitukuke,” idatero nduna ya zachuma, Simplex Chithyola Banda.
Angakhale a Chakwera atsimikizira akuluakuluwo zakuika njira zopititsira chuma cha Malawi pa tsogolo, ngongole ya dziko la Malawi pakadali pano ili K15.1 Trillion.
Pakadali pano palinso malipoti otu akuluakulu ena a boma akukhudzidwa ndi mchitidwe osakaza chuma komanso kumasainira migwirizano yomwe ikubetsa chuma chadziko lino yomwe ili misonkho ya a Malawi omwe pakadali pano akuvutika ndi kukwera mitengo kwa zinthu.