Apolisi ena adandaulidwa ku Mzimba kuti akugwirizana ndi akuba

Advertisement
Mzimba

Pakati pa mwezi wa June ndi July, 2024 anthu m’boma la Mzimba anavutika kwambiri ndi anthu akuba mowopseza pomwe anthu ena ochita malonda adavulazidwa.

Ndipo anthu awiri akugwira ukaidi kamba kopezeka olakwa pa milandu ya kuba. 

Ngakhale kuti bwalo la milandu linagwirapo ntchito yake, anthu ena ku Mzimbako akufuna a polisi awiri omwe akuti amagwirizana ndi mbavazi kuti amangwidwe. 

Anthuwanso akufuna

munthu wina yemwe amalondolera akuba-wa mu nyumba za anthu ochita malonda kuti naye akayankhe mulandu.

Malawi24 yakhala ikuchita kafukufuku pa nkhaniyi pomwe zimadziwika kuti apolisi enawa akukhuzidwa ndi umbava ndi umbanda omwe unachitika pakati pa mwezi wa June ndi July 2024.

Kafukufuku wathu tapeza kuti pali apolisi awiri omwe akukhuzidwa kwambiri ndi umbava ndi umbandawu ndipo kuti adapindulanso ndi ndalama zomwe zinabedwa kwa anthu anayi wochita malonda pa Mzimba.

Apolisiwa malingana ndizifukwa zina maina awo tawabisa.

Poyankhulapo pa nkhaniyi, katswiri wa nkhani za chitetezo Sheriff Kaisi yemwe ali Kwalalumpha wati ndi okhumudwa kwambiri kuti anthu omwe adapatsiwa mphamvu zoteteza katundu ndi miyoyo ya wanthu azigwirizana ndi mbava.

” Ndizomvesa chisoni ndithu kuti munthu yemwe ntchito yake ndiyoteteza anthu ndi katindu wawo kumachita m’chitidwe wakubanso, aka sikoyamba kumva nkhani ngati zimezi, ndimowe zililimu pakufunika kuti akulu akulu apolisi achitepo kanthu ndipo nkhaniyi asayichepetse ndithu. A polisi otelewa siofunikaso ndithu chifukwa ndiomwe akuononga mbiri ya anzawo,” Kaisi anatero.

Peter Kalaya yemwe ndi m’neneri wapolisi m’dziko muno wati malamulo salola kuti apolisi azichita nawo m’tchitidwe wakuba kapena kugwirizana ndi akuba.

“Ntchito ya wapolisi ndikuteteza katundu wa anthu ndiye ngati anthu ena ali ndi maumboni akuti apolisi ena ku Mzimba akukhudzidwa ndi umbava ndi umbanda abwere ndithu ku ma ofesi athu ndipo lamulo lizagwira ntchito,” anatsindika Kalaya.

Anthu M’boma la Mzimba kuyambira mwezi wa June mpaka pano akukhalabe mwamantha chifukwa chakuchuluka kwa umbava ndi umbanda.

Advertisement