Mlembi wankulu wa chipani cha United Transformation Movement (UTM) Patricia Kaliati, wayamikira malemu Bingu wa Mutharika komaso mchimwene wawo Peter Mutharika ponena kuti anachita chamuna popititsa chuma cha dziko lino patsogolo kuyelekeza ndi ulamuliro wa pano.
Kaliati yemwe amayankhula mu pologalamu ya padera pa wayilesi ya Zodiak, wati malemu Bingu anabweretsa m’dziko muno ndondomeko zosiyanasiyana zomwe zimayika miyoyo ya aMalawi patsogolo, monga chidwi chake pa nkhani ya feteleza wotsika mtengo.
Mwachitsanzo iwo ati, “Peter anafikira nambala imodzi pa zachuma chifukwa choti anachepetsa ngongole, ifeyo tikuchulutsa ngongole kwambiri. Tikunena pano ofesi ya Accountant General kuli ngongole ya K110 biliyoni yomwe ikulepheleka kupelekedwa kwa anthu omwe anapuma pa ntchito. Lero munthu amene anapuma pa ntchito 2022 akulandira ndalama 2024 chifukwa choti kulibe ndalama. Panopa Malawi tili ndi ngongole ya K10.6 thililiyoni.”
Iwo anawonjezera kuti zinthu zambiri m’dziko muno zikumasokonekera kwambiri kamba koti atsogoleri pano akumalowetsa ndale nkhani za chitukuko zomwe ati ndizolakwika.
Kuwonjezera apo, Kaliati wadzudzula kuchuluka kwa ma ulendo omwe mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera akuyenda m’dziko muno komaso kupita mayiko akunja ponena kuti zathandizira kuwononga chuma cha dziko lino.
“Chomwe tikufunika ife kuti chuma chiyende bwino pakufunika kuchepetsa ma ulendo. Bingu anachita bwino Peter anachita bwino chifukwa ma ulendo anali ochepa, sanawonjeze kuchulukitsa maulendo. Ma ulendo a m’dziko momuno ngakhaleso opita mayiko akunja aja timaononga ndalama zambiri,” watelo Kaliati.
Iwo ati ngati chipani cha UTM chingalowe m’boma chaka cha mawa chino, chidzawonetsetsa kuti chikubweretsa ndondomeko zosiyanasiyana zokomera a Malawi onse.