Ndalama ya 20 Kwacha ikupitilira kukanidwa madera ena ku Lilongwe

Advertisement
Lilongwe

Ngakhale kuti Bank yayikulu m’dziko muno ya Reserve, idachenjeza anthu ochita malonda ang’ono an’gono kuti asamakane ndalama ya 20 Kwacha, madera ambiri ku Lilongwe akupitilira kuyikana ndalamayi.

Gift Mbetewa yemwe amachita malonda ogulitsa mowa ku Chilinde mu mzindawu wati iye amakana 20 Kwacha chifukwa ma shop ena akuluakulu komwe amaoda katundu monga fodya amawakana.

“Ngati ma shop akuluakulu omwe ife timadalira kuoda katundu akukana nde ifenso ndizotivuta kuti tingalole 20 Kwacha,” iye anatero.

Prince Makowa yemwe amapanga malonda a taxie ku City Centre anati iye ma 20 Kwacha amalandira koma vuto likumakhala kwa anthu ena akumayikana akamawapasa chenje.

“Ine ndimalandira chifukwa olo ndipite pa malo omwetsera mafuta ndalamayi imaloledwa ngakhale kuti makasitomala ena ambiri amayikana tikamawapasa chenje,” anafotokoza Makowa.

Poyikirapo ndemanga oyankhulira Bank ya Reserve a Mark Lungu awuza Malawi24 kuti ndalama yomwe Bank-yi sinachotse ikuyenera kugwira ntchito kaya ndi 20 kwacha kaya ndiyachitsulo.

“Ndi apemphe aMalawi omwe akupanga malonda osiyanasiyana kuti ndalamayi azilandira chifukwa sinasiye kugwira ntchito, anthu amene akukana ndalamayi akulakwa,” anamema chotero.

Lungu anapitlira kufotokoza, “Posachedwapa tayendapo kuchokera ku Nsanje mpaka ku Chitipa kuchititsa misonkhano maka malo ochitira malonda kuwauza anthu kuti asakane 20 olo 50 Kwacha ndipo sitisiyira pomwepo.”

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.