Tiyenda maliseche – aopseza amayi a DPP

Advertisement
Democratic Progressive Party - DPP

Poyenda mtaunimu kumayenda osamalitsa, penanso olo mutatsinzina kumene. Pali chiopsezo choti amayi a chipani chotsutsa cha DPP tsiku lina mutha kukumanizana nawo adakali chibadwire.

Amayi otsatira chipani cha DPP ndinso mtsogoleri wakale a Peter Mutharika ati ayenda mbulanda kupita kunyumba ya boma ngati lingaliro lofuna kumunjata Peter Mutharika lingapitilire. Amayiwa anena izi pa nkumano wawo omwe anachita mu mzinda wa Blantyre lachisanu pa 2 August.

Malinga ndi Mayi Maria Mainja amene analankhula pa mkumanowu, ati boma likuzembelera kufuna kunjata a Mutharika. Iwo adagwira mawu a nyuzipepala ya Nation yomwe idalemba za ndondomeko yofuna kunjata a Mutharikayi kamba ka nkhani yokhuza Blue Night.

“Taona kuti akufuna amange a Mutharika ndi kuthetsa chipani cha DPP,” anatero a Mainja. “Komatu ayerekeze, ndikuti angoyerekeza kumuyandikira Mutharika, ife ndiye kuti tichite chionetsero choyenda malipsata.”

Pamene Mayi Mainja amanena izi ndiye kuti amayi anzawo mmbalimu akuyimba nthungululu ndi kuyipatsa moto kusonyeza kuti ndi okonzeka kuyenda chibadwire pofuna kusonyeza mkwiyo wawo.

A Mainja, amene ndi wamkulu wa amayi ku chigawo chakummwera mu chipanichi, adati a Kongeresi akuopa kuthidzimulidwa ndi APM pa chisankho chaka chamawachi ndiye angoganiza zomuthira unyolo basi.

Nyuzipepala ya Nation idanena kuti mabungwe omwe si aboma apempha bwalo kuti lithetse chipani cha DPP ndinso kunjata atsogoleri ake chifukwa sanabwenze ndalama zomwe adapatsidwa ndi kampani za boma mu chaka cha 2017 kupanga mwambo wa Blue Night.

Advertisement

One Comment

  1. Ingomulipililani ndalamazo basi apo biii akaliwatu

Comments are closed.