Chiyanjano Mbeza apitilira kugona mchitokosi

Advertisement
Chiyanjano Mbeza

Nkozi wa nyimbo Chiyembekezo Mbeza yemwe akuganizilidwa kuti wakhala akufalitsa mauthenga opatsa mantha komanso onyoza mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, agonanso mchitokosi kufikira Lachisanu pomwe bwalo la milandu likapeleke chigamulo pa pempho la belo. 

Mbeza yemwe adamangidwa Lolemba madzulo, Lachitatu anaonekera ku bwalo la milandu munzinda wa Lilongwe komwe woimira boma a Charles Panyani anauza bwalolo kuti mkuluyu amumanga ndikumulanda zida zina zomwe amagwiritsa ntchito.

Panyani wati kafukufuku wawo akusonyeza kuti Mbeza pamodzi ndi anthu ena, wakhala akufalitsa mauthenga opatsa mantha komanso odzetsa chisokonezo zomwe akuti ndikuphatikizapo mauthenga onyoza mtsogoleri wa dziko lino Chakwera.

Panyani anapempha bwaloli kuti Mbeza apitilire kusungidwa mchitokosi kwa masiku asanu ndi awiri (7) kuti mbali ya boma itsilize kafukufuku wake yense pa nkhaniyi.

Koma yemwe akuyimilira Mbeza pa mlanduwu anatsutsa pempholi ponena kuti kupanga zimenezo ndikulakwira malamulo kamba koti apolisi amayenera ayambe afufuza kaye mokwanira ndikupeza maumbonu asanamumange oganizilidwayu.

Apa oweruza milandu Roderick Michongwe, wati apeleka chigamulo pa pempho la belo la Mbeza Lachisanu lino pa 26 July.

Chiyanjano Mbeza yemwe ndi mwini wake wa CIA Studio, amachita bizinezi yojambula nyimbo ku HHI munzinda wa Blantyre ndipo akuganizilidwa kuti ali mgulu la anthu omwe amajambula ndikutulutsa nkhani zosiyanasiyana pa tsamba la Bakili Muluzi TV.

Advertisement