Kumbukirani kupemphelera dziko lathu – Chakwera

Advertisement
Chakwera

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ati mpingo uli ndi gawo lalikulu kupemphelera dziko la Malawi ndi masomphenya ake.

M’mawu awo pamene anakasonkhana nawo pa mwambo wa mapemphero ku mpingo wa Lingadzi CCAP mu mzinda wa Lilongwe a Chakwera anati mpingo ukuyenera kupemphelera dziko lathu ndi masomphenya a tsogolo lake, Ponena kuti aliyense akuyenera kudzidalira payekha komanso kutumikira ena.

Mtsogoleri wa dzikoyu wati anthu akamapemphelera mpingo ndekuti mpingo umatukuka komanso mwa njira ina dziko limatukuka ndi kuyima palokha chifukwa mipingo ndi yomwe ikusunga anthu amene ndi nzika za dziko.

Pophera mphongo mutu wa mtsiku la lero pa mpingowu woti ‘ndine oyang’anira wa m’bale wanga,’aChakwera ati pamene zinthu zina sizinayende bwino m’moyo uno tisamachitire mwano mulungu.

Mu uthenga wawo abusa a mpingowu, a Davie Franklin Salimoni anati mkofunika kuti anthu adzipemphelerana wina ndi nzake ponena kuti uwu ndi udindo wa aliyense amene amapemphera.

Advertisement