Oyimba Ethel Kamwendo, San B ndi Collen Ali sakhutisidwa ndi World Music Day ku Malawi

Advertisement
Ethel Kamwendo

Lero pa 21 June ndi tsiku lomwe linakhazikitsidwa mwapadera padziko lonse kuti anthu azikumbukira ubwino wa nyimbo, pobweletsa pamodzi zamba zosiyanasiyana.

Koma oyimba ena asonyeza kusakhutitsidwa ndi momwe tsikuli limakhalira kwathu kuno.

Malawi24 inachita mwayi oyankhulana ndi ena mwa an’khala kale pa nkhani zamayimbidwe m’dziko muno kuti afotokoze m’mene tsikuli amalikumbukilira kwathu kuno.

San B
San B

“Ndimasangala kuti tsikuli linakhazikitsidwa koma kwathu kuno palibe sapoti yomwe ndimayiona kuchokera kwa adindo, akakhala masiku ena omwe amakumbukilidwa zambiri zimachitika ndipo boma limayenera kutenga gawo,” anatero San B.

Nayenso Ethel Kamwendo anafotokoza mbali yake kunena kuti chiyambireni kuyimba sakhutisidwa ndim’mene tsikuli limatengeredwa.

“Taonani lero kuli ziiii!! ngati palibe chochitika,”ananyinyirika.

Collen Ali
Sindimadziwa kuti lero ndi World Music Day – Ali.

Titayankhula ndi Collen Ali katswiri amene wajambulapo nyimbo za oyimba odziwika bwino monga Lucius Banda, Billy Kaunda komanso ena ambiri mu zaka za m’ ma 90’s anaoneka odabwa titamufunsa za tsikuli.

“Zoti lero ndi World Music Day mukundiuza ndiinu ine sindikudziwa chilichonse, zomwe zikusonyeza kuti palibe chomwe chimachitika kwathu kuno zokhuza tsikuli,” iye anatero.

Pakuyankhapo, mlembi wamkulu wa bungwe la MUM a Tonney Chitimatima anati mwambo okumbukira tsikuli unakakhalapo lero koma wasunthidwa kufikira pa 29th August, kupereka ulemu kwa abale 9 omwe anatisiya pa ngozi ya ndege lolemba tsabata latha.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.