
Ana ongoyendeyenda (street kids) asumila m’modzi mwa oyimilira milandu Sylvester Ayuba James pa zomwe analemba pa tsamba lake la mchezo zokhudza anawa.
Pa 14 January, 2025, a James analemba pa tsamba lake la mchezo kupempha Boma kuti liziwombera ana omwe amavutitsa anthu maka kuwabera mu mzinda wa Lilongwe.
Mukalata yawo yomwe alemba kudzera mwa omwe akuwayimilira ndipo ayitumiza ku bungwe la Malawi Law Society ndi Malawi Human Rights Commission, anawa akuti zomwe analakhura a James zikuyika moyo wawo pa chiwopsezo kuphatikiza ana ena omwe samapanga nawo zakubazo.
” Enafe timapita ku nsewu ndi cholinga choti tikapemphetse komanso kukapeza maganyu kuti tipeze chakudya pa moyo wa tsiku ndi tsiku, choncho zomwe analakhura Ayuba ndi zopeleka mantha kwa ife maka omwe sitipanga zakuba,’ iwo anatero.
Ayuba anati anawa omwe anawatchula kuti akuba komanso ana oopsa akuwononga nyale za mu msewu komanso akumamenya ndi kubera anthu kukada.
Iwo anati ngati a Boma akufuna kubweretsa bata mu mzindawu choyamba ndikubweletsa anthu omwe azikhala ndi mifuti kuti aziwombera ana akubawa usiku ndikukawakwilira ku boda ya Mozambique ku Dzalanyama kapena kukawaponya ku afisi a ku Thuma game reserves.
Koma mukalata yawo anawa akuti Ayuba James kukhala lawyer samayenera kulemba zinthu ngati zimenezi, ndipo apemba bungwe la Malawi Law Society kuti lilowerepo powenetsetsa chitetezo chawo.
Poyakhapo Ayuba James anati ngati anawa alembera bungwe la Malawi Law Society ndekuti si ana oyendeyenda, koma kuti ndi kagulu ka anthu kena komwe kali ndi zolinga zina.
M’neneri wa Malawi Law Society a Gabriel Chembezi anati anakafufuzabe za kalata yomwe yalembedwayo.
Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) Micheal Kaiyatsa anati zomwe analemba Ayuba James ndi zosakhala bwino komanso zoyika moyo wa ana oyendeyenda pa chiwopsezo.
Poyankhapo pa kalatayi mkulu wa Malawi Human Rights Commission ( MHRC), anati akutsatira bwino nkhaniyi ndipo owona za Malamulo Ku bungweli akuyiwona nkhaniyi.
Miyezi yapitayi magetsi a solar omwe anayikidwa mu nsewu wa Lilongwe akhala akuwongedwa komanso kubedwa ndi anthu osadziwika bwino.
Mu mzinda omwewunso anthu akhala akuchitidwa chipongwe maka pa ABC ndi ana oyendayenda (street kids).