BBC Itipepese – aMalawi

Advertisement
Saulos Chilima

Nyumba yosindikiza nkhani ya m’dziko la United Kingdom ya British Broadcasting Company (BBC), yawonjezera mkwiyo komaso chisoni cha a Malawi pomwe yanena kuti malemu Saulos Chilima anazengedwapo milandu ya katangale m’boma.  

Lachiwiri, BBC Africa yatulutsa nkhani momwe ikukamba za moyo wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino malemu Chilima omwe afa pamodzi ndi anthu ena asanu ndi atatu pangozi ya ndege.

Mwazina, BBC Africa kudzera kwa wolemba nkhani wawo Basillioh Rukanga, yati ngakhale Chilima anali wolimbikira ntchito, koma ankadziwika ngati munthu yemwe anali patsogolo kuchita katangale m’boma.

Mbali ina ya nkhaniyi yati, “Ngakhale ankanenedwa kuti ndi wochita zinthu modzipeleka komaso wokonda kugwira ntchito, koma ankadziwika kuti ndi amene anali patsogolo pa nkhani za ziphuphu m’boma.”

Nkhaniyi yomweso yayikidwa pa tsamba la fesibuku la BBC Africa, yatokosora mkwiyo wa a Malawi omwe akhamukira ku tsambali komwe akuyidzudzula ponena kuti a Malawi ambiri ali ndi chisoni pa imfa ya Chilima ndi anthu ena 9 ndipo nkhani yotele siyoyenera pa nthawi ino.

Poyikira ndemanga mchingerezi, Samantha Mphongo wauza BBC Africa kuti “Tiloleni tiwalire (malemu Chilima) popanda inu kubweretsa nkhani zoduka mutu pa nthawiyi. Kwa ife Amalawi, tataya mtsogoleri wamkulu, ndipo mwina mungafunike kukumbutsidwa kuti milandu yake yonse idathetsedwa.”

Munthu wina wawuzaso nyumba yosindikiza nkhaniyi kuti malemu Chilima ndi munthu yemwe sadzaiwalidwa kamba kakulimbikitsa achinyamata kukhala patsogolo pa nkhani yolamulira dziko.

“Iye (Chilima) anali ngwazi yathu. Anayimilira achinyamata ndipo anatilimbikitsa kuti titengepo mbali pa kayendetsedwe ka dziko lathu. Adayimira maloto a achinyamata aku Malawi ndipo adatiuza kuti tigwire ntchito molimbika.

“Izi ndi zomwe Saulos Klaus Chilima anali kwa ife. Mutha kumuyipitsa koma kwa ife sanali munthu wamba ameneyo. Anali purezidenti wathu,” watelo EL Stonewall Kukomoka poikira ndemanga pa nkhaniyi.

Anthu ambiri omwe athilira mlomo pa nkhaniyi pa tsambali ati akufuna BBC Africa ipepese komaso ifufute nkhani yomwe yasindikizayi ponena kuti nkhaniyi ndichitozo ku dziko la Malawi.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.