Yomwe idathibula Wanderers nayo yathibulidwa

Advertisement
Fomo Fc vs Mzuzu City Hammers

Mzuzu City Hammers yagonja ndi timu ya Fomo Fc pamasewero omwe anamanga nthenje lero pa bwalo la masewero la Mulanje pophaphalitsidwa ndi zigoli ziwiri kwa chimodzi.

Fomo inapeza chigoli pa mphindi zisanu ndi zinayi kudzera mwa nyamata ameneyu Hassan Luwembe amene anakunga chigoli chochititsa kaso kwambiri.

Mchigawo choyamba chomwecho Hassan Luwembe anadzagoletsa chigoli chachiwiri pa mphindi zokwana makumi awiri ndi ndi imodzi kupangitsa Fomo kutsogola ndi zigoli ziwiri kwa duu.

Nayo Mzuzu City Hammers itaona kuti ayibatiza nazo zigoli, nayo sinachitire mwina koma kupeza chigoli kudzera pa penate yomwe anafumphula ndi Isaac Msiska, osewera emwe adachinyanso zigoli ziwiri sabata latha.

Zitakwana mphindi zokwana makumi anayi ndi zisanu, oyimbira maswero anakoka wezulo kuti chigawo choyamba chatha kamweni kaye madzi.

Mchigawo chachiwiri palibe amene anagoletsa, ndipo nthawi itakwana oyimbira anakoka wezulo kuti zathapo basi.

Ayi ndithu Fomo yapeza chipambano pogoletsa zigoli ziwiri pamene, Mzuzu City Hammers inapeza chimodzi kusonyeza kuti yagonja pa masewero amenewa.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.