Wangotamanga Ramadhani, Noma yatola chipambano kwa Dedza Dynamos

Advertisement
Premier Bet Dedza Dynamos

Timu ya Mighty Mukuru wanderers lero yachita chamuna kupambana pa imodzi mwa ma timu amene amavutana nawo kwambiri ya Premier Bet  Dedza Dynamos ndi zigoli zitatu kwa chimodzi.

Osewera kutsogolo wa timu ya Manoma  Christopher Kumwembe ndi amene anayamba kubweletsa mkuwe pa bwalo la Kamuzu mu mzinda wa Blantyre atagoletsa  chigoli  ndi mutu pa mphindi  yachitatu asanabwere Chifuniro Mpinganjira pa mphindi ya chi 20 kuti akapumulire chigawo choyamba  ili 1-1.

Mighty Mukuru wanderers
Mighty Mukuru wanderers yagonjetsa Premier Bet Dedza Dynamos

Mphunzitsi Meke Mwase yemwe anali wachiwiri kwa Nswazurimo Ramadhani asanayisile ntchitoyi panjira analowetsa Isaac Kaliati mchigawo chachiwiri ndipo mphindi yachisanu mchimodzi anakoleka kutsogozanso anyamata a ku  nseu wa Lali  Lubani ku Blantyre.

Kaliati anaona kuti ziwiri ndi zosakwana anabweranso kumalizitsa mpira wa pakona omwe anamenya Stanley Sanudi ndipo Vincent Nyangulu anasumba kuti ulowe koma polimbalimba Kaliati anangomalizitsa kuti apakile zigoli ziwiri mthumba mwake.

Pamapeto pa zonse Mighty  Mukuru Wanderers 3-1 Premier Bet Dedza Dynamos Isaac Chair’ Kaliati anasankhidwa ngati osewera wapamwamba m’masewelowa.

M’mawu ake mphunzitsi wa Wanderers Meke Mwase wati anali okondwa ndi chipambano ndipo anakhulupilira anyamata ake kuti apeleka chipambano.

Mphunzitsi wa Dedza Andrew Bunya wati  ukadaulo wawo opambanira omwe anakonza kuti agonjetsele wanderers unakanika kugwira ntchito ngakhale anasintha kangapo  ndipo agoletsetsa zigoli zomwe samayenera.

Zatelemu Manoma yatolera ma point onse atatu kuti ifike pa ma pointi 15 mu masewelo 9, ndipo Dedza idakalibe ndi ma pointi 8 mu masewelonso 9.

M’masewelo ena, FOMO yagonjetsa Mzuzu City Hammers 2-1, zigoli za Hassan Luwembe ziwiri ndi Isaac Msiska, MAFCO yagonja 2-1 kwa Creck Sporting club zigoli zochoka kwa Peter Kasonga, Gift Kadawati ndi Yasin Chida, ndipo Moyale Barracks yaswa Mighty Tigers ndi Chigoli chimodzi kuchokera kwa Raphael Phiri.

Advertisement