Sitikugwetsanso Kwacha – yatsutsa RBM

Advertisement
Reserve Bank of Malawi

Banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve (RBM) yatsutsa mphekesera zomwe zikumveka kuti ikufuna ichepetseso mphamvu za ndalama ya dziko lino.

Nkhaniyi ikudza pomwe pamasamba a mchezo pakhala pakuzungulira mphekesera yoti RBM ikufuna kutsitsanso mphamvu ya ndalama ya Kwacha kumapeto a mwezi uno.

Mphekeserazi zimasonyeza kuti bankiyi ikufuna kugwetsa mphamvu ya ndalama ya dziko lino ndi 30 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse.

Koma poyankhula ndi nyumba zina zofalitsa nkhani m’dziko muno, ofalitsa nkhani ku RBM a Mark Lungu ati mphekeserazi ndi bodza la mkunkhuniza.

A Lungu ati a Malawi asadele nkhawa kamba koti bankiyi ilibe ilibe malingaliro aliwose ofuna kutsitsanso mphamvu ya ndalama ya dziko lino.

Ndalama ya Kwacha inachepetsedwa mphamvu komaliza pa 9 November chaka chatha ndi ndi 44 Kwacha pa 100 Kwacha iliyonse.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.