Dziko la Malawi tsopano Lili ndi mkulu wa kalembera wa zipani watsopano

Advertisement
Kizito Tenthani

A Dr. Kizito Tenthani tsopano ndi mlembi wa zipani zandale m’dziko muno.

Izi zikudza kutsatira kuvomelezedwa kwa a Tenthani pa udindowu ndi nyumba ya malamulo.

Potsimikiza za nkhaniyi, m’khalapampando wa komiti yosankha anthu m’maudindo osiyanasiyana a boma ku nyumba ya malamulo a Joyce Chitsulo adati ndi okhutira ndi kusankhidwa kwa a Tenthani pa udindowu ndipo anati ali ndi chiyembekezo kuti a Tenthani agwira ntchito yawo mwaukadaulo komanso modzipeleka.

Joyce Chitsulo
Ndife okhutira ndi kusankhidwa kwa a Tenthani – Chitsulo.

Mwa zina, a Chitsulo anati ali ndi chiyembekezo kuti a Tenthani awonetsetsa kuti akulimbikitsa lamulo la zipani zandale lomwe mwa zina limaletsa zipani zandale kugawa katundu osiyanasiyana kwa ozitsatira ake ngati njira imodzi yokopera anthu.

A Chitsulo adatinso akuyembekezera kuti zipani za ndale ziwonetsetsa kuti zikubweletsa pa mbalambanda njira zomwe zipanizi zimapezera chuma chake.

A Tenthani adapambana mayeso omwe bungwe la Civil Service Commission lidachititsa mu mwezi wa January chaka chino.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.