A Chakwera akulowela nawo achinyamata ku thengo – watelo kafukufuku

Advertisement

Zangolunjikana ndi sabata yomwe boma laganiza kuchotsa milandu yokhudza za Katangale  ya wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko la Malawi a Saulos Chilima ngakhale bungwe lothana ndi Katangale la Anti- Corruption Bureau (ACB) linati lili ndi ma umboni okwanila a zakatangale zomwe a Chilima adachita.

A chilima amayimbidwa mulandu woti adalandira chiphuphu kwa wakatangale ochita malonda Zuneth Sattar. Ndipo kuthetsa milandu ya aChilima anthu sakudabwa malingana ndi m’mene Katangale wakulira ku Malawi pakali pano kufika pa mulingo okhazika chete mkulu wa nthambiyi a Martha Chizuma.

Zotsatira za kafukufukuyu zakumana chindunji kuti Malawi akulowera ku phompho la ngozi pamene posachedwapa mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera anaikira kumbuyo a kamuna anayi ogwira ntchito m’boma limodzi ndi akazi awo pamene America idati asadzapitenso m’dziko lawo kamba kokhudzidwa ndi zakatangale ndi Sattah koma a Chakwera anati kukaniza makosanawa mkulakwa komanso nzoseketsa ponena kuti nalo dziko la America lili ndi milandu ya katangale ya mbwee.

Mkuona kwa diso la wamba pa zomwe zikuchitika m’dziko lino sizodabwitsa kuti kafukufukuyu wa “African Youth survey” wati tsogolo la achinyamata m’dziko lino pansi pa utsogoleri wa a Chakwera likulowera ku matsitso a ngozi.

Kafukufukuyu anachitikanso mu mayiko ena mu Africa monga Rwanda, Ghana, Kenya, Zambia, Nigeria , Mozambique ndi South Africa omwe nawo zaonetsa mayankho onga a ku Malawi.

Advertisement