Chipatala cha Mzuzu chikuwumiliza odwala kuti azilipira thandizo la opareshoni-kafukufuku

Advertisement

Odwala omwe akufuna kupeza thandizo la mankhwala pa chipatala chachikulu cha Mzuzu awulura kuti ogwira ntchito ena akuwumiliza odwalawa kulipira ndalama ngati akufuna kuthandizidwa mwachangu pofuna kupangidwa opareshoni pa chipatalachi.

Malingana ndi kafukufuku yemwe Malawi24 inapanga, zikuwonetsa kuti odwala ena atha miyezi yoposa inayi asanapatsidwe thandizo la mankhwala, pomwe ena akulandilandira thandizo ngati lomweri akalipira, odwala wina anafotokoza.

Mayi wina amene timutchule kuti mayi Juliet Nkhoma mundimeyi akufotokoza momwe akukanikira kulandira thandizo la opeleshoni atapangidwa opareshoni koyamba mu mwezi wa October chaka chatha yomwe siinayende bwino, ndipo wakhala akuyembekezera kupangidwaso opareshoni ina kuyambira mwezi wa January chaka chino, koma mpaka pano sanathandizidwebe.

 “Ndinabwera kudzabereka mwana wanga wachiwiri mu October, ndipo a dokotala anandiuza kuti ndikuyenera kupangidwa opareshoni zomwe ine ndi amuna anga tinavomereza, patangotha miyezi iwiri atandipanga opareshoni sindimamva bwino mthupi ndipo ndinabwera kuchipatala kuno kuti andiunike, ndipo anandiuza kuti ndili ndivuto loyenera kupangidwaso opaleshoni.” 

“Kuchokera mwezi wa January sanandipange opareshoni, ogwira ntchito amangondisinthira masiku a opareshoni ponena kuti alibe zipangizo zopangira opereshoni, chodabwitsa ndichakuti, ndimaona anthu akulandira thandizo ngati lomwero ndipo nditafunsa m’modzi mwa akulu akulu ogwira ntchito kuno anandiuza kuti sindingalandire thandizo mwamsanga ngati palibe ndalama zopatsa a dokotala, anatero a Nkhoma.

Tinalankhulaso ndi bambo Nelson Makwinja omwe akudikiraso kupangidwa opareshoni atapezeka ndi chotupa m’mimba ndipo iwo anati atha pafupifupi mwezi osathandizidwa pachipatapa.

“Ndinabwera mwezi wa Malichi ndipo ndikungopatsidwa mankhwala ochepetsa uluru, ndikawafunsa, samandipatsa mayankho ogwira mtima, pamene ena omwe anabwera pambuyo panga adathandizidwa dnikumapita ndipo ine ndikungosungidwabe chifukwa mwina ndilibe kalikonse koti n’kupatsa a dokotala kuti ndilandire thandizo,” anatero a Makwinja.

Koma polankhura ndi m’neneri wa pachipatalichi a Arnord Kayira, anakana kuti chipatalachi chikukakamiza odwala kupereka ndalama kuti alandire thandizo.

 “Sizoona kuti pachipatala pano tikukakamiza odwala kuti alipire asanalandire thandizo la mankhwala, kupatulako ku nthambi yolipilitsa yokha basi,” iwo anatero.

Anapitiliza kufotokoza kuti odandaula akuyenera kukanena kunthambi yomva madandaulo la ombudzman kapena bungwe lothana ndi ziphuphu la anti-corruption, anafotokoza a Kayira.

Advertisement