Anthu alimbikitsidwa kugwiritsa ntchito njira zingapo zopewera kutenga HIV

Advertisement
hiv-ribbon

Pomwe zotsatira za kafukufuku zasonyeza kuti anthu opitilira 15,000 ndi omwe anatenga kachirombo ka HIV chaka chatha chokha, akatswiri ati kugwiritsa ntchito njira zingapo zopewera kutenga kachiromboka, kungathandize kuchepetsa chiwerengerochi.

Izi ndi malingana ndi a Ulanda Mtamba omwe ndi wa chiwiri kwa mtsogoleri wa bungwe la Civil Society Advocacy Forum omwenso ndi m’modzi mwa akatswiri omwe akutsogolera kampeni yotchedwa ‘CHOICE’.

A Mtamba ayankhula izi Lachisanu pa 19 April, 2024 munzinda wa Blantyre pomwe bungwe la Journalists Association Against AIDS (JournAIDS) mogwirizana ndi bungwe la AVAC linachititsa maphunziro a atolankhani pa nkhani yokhudza jakiseni wa PrEP yemwe wayamba kupelekedwa m’zipatala zina mdziko muno. 

Iwo anati ndikofunika kuti pa chisankho chomwe munthu angapange pa njira zomwe angatenge pofuna kupewa kutenga ka chirombo ka HIV, adzionjezeraposo njira ina yapadera.

Iwo anati kupanga izi kutha kuthandiza kuti munthu asamakhale pa chiopsyezo chotenga ka chirombo ka HIV pomwe njira imodzi yopewera yomwe anatenga yalephera kugwira ntchito yake moyenelera.

Apa mayi Mtamba anapeleka chitsanzo choti munthu amene wasankha njira yopewera kutenga ka chirombo ka HIV yakumwa PrEP, athaso kugwiritsa ntchito chishango pa nthawi yomwe akuona kuti ali pa chiopsyezo chotenga ka chiromboka.

“Tikayang’ana ka chirombo ka HIV, umapeza kuti njira imodzi imatha kukuteteza mbali ina, njira ina imatha osakuteteza mwina ku matenda opatsirana pogonana. Nde kwambiri timalimbikitsa kuti munthu adzitha kukhala ndi chisankho chosankha njira yodzitetezera.

“Komaso ngati njira zinazo angakwanitse kuziphatikiza, agwiritse ndithu njira zingapo, tisangotsamira njira imodzi; chifukwa imodzi imeneyo ikakhala kuti yalepheleka nde kuti amakhala kuti munthu uja adakali pa chiopsyezo,” watelo Mtamba.

Kuwonjezera apo, a Mtamba ati palinso chiyembekezo choti chiwerengero cha anthu atsopano omwe akutenga HIV chitha kutsika kwambiri kamba ka kubwera kwa jakisoni wa PrEP yemwe akugwira ntchito yofanana ndi PrEP wakumwa pakuteteza anthu kutenga kachilomboka.

M’mawu ake, Dingaan Mithi yemwe ndi m’modzi mwa akuluakulu a bungwe la JournAids, ati maphunzirowa anakozedwa pofuna kuphunzitsa olemba nkhani za kuthekera komwe jakiseni wa PrEP ali nako pa ntchito yochepetsa chiwerengero cha anthu atsopano omwe akumatenga ka chirombo ka HIV.

A Mithi ati ali ndi chiyembekezo kuti maphunzirowa athandiza olemba nkhaniwa kukhala ndi ukadaulo pakalembedwe kabwino ka nkhani zokhudza jakiseni wa PrEP komaso nkhani zokhudza ka chirombo ka HIV.

Zina mwa njira zomwe a zaumoyo anavomeleza ndipo amalimbikitsa anthu mdziko muno pofuna kupewa kutenga ka chirombo ka HIV ndi monga; kukhala okhulupilira, kudziletsa, kugwiritsa ntchito zishango, mdulidwe wa a bambo wa ku chipatala, kumwa PEP ndi PrEP komaso PrEP wobaya yemwe wafika kumene. 

Advertisement