Awiri anjata pofuna kulowetsa chamba ku ndende

Advertisement

Mnyamata wina yemwe amayankha mlandu kale, wamangidwaso kachiwiri pamodzi ndi mzake wina yemwe amafuna kukamupatsira chamba chomwe anachibisa munkhwayira tsiku lakumva mlandu.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa Polisi ya Zomba, a Patricia Supuliano, oganizilidwa awiriwa ndi Estery Evance wa zaka 19 komaso Bonface Phiri wa zaka 22.

 A Supuliano ati izi zachitika Lachiwiri pa 16 April, 2024 pomwe a Phiri anali ku bwalo la milandu komwe amayankha mlandu wina ndipo akuti Evance anapita kukamvera mlanduwo.

 Ofalitsa nkhaniyu wati Evance adanyamula nkhwaila zowoneka mokayikitsa kwambiri zomwe amafuna awapatsire a Phiri  akamabwelera ku ndende ya Zomba komwe amawasunga podikira chigamulo cha mlandu wawo.

Kamba kokayikira ndi maonekedwe a nkhwayirazo, a Polisiwo anamulanda Evance ndi kuzitenga kuti aziwonetsetse ndipo akuti apapa ndi pomwe anapeza pansi pake atachinyiza chamba.

 Apolisi atazindikira za matcherawa, sanachedwe koma kuthira zingwe makosana awiriwa ndipo zatelemu, a Phiri awonjezera mlandu wina pa oyamba omwe amayankha.

 Evance pamodzi ndi Phiri, onse akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu apezeka ndi chamba popanda chilorezo. 

Advertisement