Njovu yapha mayi ku Dedza

Advertisement
Malawi 24 news logo

Njobvu imodzi mwa ziwiri zomwe zinatuluka m’nkhalango ina m’boma la Dedza, yapha mayi wa zaka 45.

Watsimikiza za nkhaniyi ndi ofalitsa nkhani pa polisi ya Dedza, Beatrice Jefita, yemwe wazindikira malemuwo ngati a Volontina Yonasi omwe akuti akumana ndi tsokali Lachiwiri pa 16 April, 2024.

A Jefita awuza nyumba zina zoulutsa mawu mdziko muno kuti ngoziyi yachitika m’mudzi mwa Chilasamungo pomwe nyama ziwirizi zinathawa m’nkhalango ya Thuma ndikulowa m’mudziwu kukadya mbewu za anthu.

Ofalitsa nkhaniyu wati anthu am’mudziwu atawona izi, anakatsina khutu apolisi  motsogozedwa ndi akuluakulu oyang’anira nkhalango anathamangira ku maloku ndicholinga choti akabwezeretse nyama zolusazi m’nkhalango ya Thuma.

Anthu a m’mudzi wa Chilasamungo, kuphatikiza malemu Yonasi, anasonkhana kuti awonerere ntchito yobwezeretsa nyamazi m’nkhalangoyi ndipo akuti ngoziyi yachitika nthawi yomwe akuluakulu oyang’anira nkhalangowa anaombera m’mwamba pofuna kuopseza njobvuzi kuti zibwerere m’nkhalangoyi.

Apolisi ati njobvuzi zitava kulira kwa mfuti, zinayamba kuthawira m’nkhalango momwe zinachokeramo koma akuti imodzi inasintha njira ndi kulunjika komwe malemu Yonasi anali ndipo kamba ka mantha, iwo anagwa pansi ndipo apa ndi pomwe njovuyi inawaponda ndi kuwapheratu.

“Ali mkati mokusa nyamazi, njobvu imodzi inalunjika komwe kunali malemuwa ndipo pofuna kuthawa a Yonasi anagwa zomwe zinapeleka mpata kwa njobvuyi kuti iwaponde,” atero a Jefita.

A Jefita atsimikiza kuti akuluakulu a nkhalangowa anakwanitsa kubwezeretsa njovu ziwirizi m’nkhalango ya Thuma.

Malemu Yonasi anali ochokera m’mudzi mwa Kaulalo, mfumu yaikulu Kamenyagwaza m’boma lomweli la Dedza.

Advertisement

Leave a Comment

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.