Tay Grin ali ku UK ndi Mutale Mwanza

Advertisement

Pomwe anthu ochuluka analavula za ku khosi zitaoneka kuti oyimba Tay Grin wasiyana ndi bwezi lake la m’dziko la Zambia, Mutale Mwanza, awiriwa ali limodzi ku United Kingdom, ndipo gulu langoti kukamwa yasa kwinaku manja ali ku nkhongo, osakhulupilira zomwe awona.

Mwezi watha, pa masamba a m’chezo, panali pokopoko kamba ka uthenga wina omwe Mwanza yemwe wakhala pa ubwenzi ndi Tay Grin kuyambira chaka chatha, analemba pa tsamba lake la fesibuku.

Uthengawu, anaulemba mosonyeza kuti wasweka mtima ndi zomwe bwenzi lake linamuchita ngakhale zifukwa zake sanapereke ndipo zinkasonyeza kuti ubale wa awiriwa ukuyenda mwa pendapenda.

“Ngakhale titasiyana nthawi ya 11 koloko, dziwa kuti imakati 11:1 koloko ndipeza wachikondi wina,” inatelo mbali imodzi ya uthengawu omwe Mutale anaulemba mchingerezi.

Izi zinapangitsa anthu kuyankhula motha mawu ndipo ambiri ankaonetsa kuti ndi zomwe akhala akuyembekezera ponena kuti samaona tsogolo lenileni pa ubwenzi wa anthu awiriwa.

Koma anthu atayankhula zonsezo, zikuoneka kuti ubwenzi wa Tay Grin yemwe amatchukuso kuti ‘Mfumu ya Zinyawu’ ndi Mutale, unakalipo kamba koti awiriwa tikuyankhula pano ali limodzi mdziko la UK komwe akupanga zinthu zina.

Aliyese mwa awiriwa wayika pa tsamba lake nchezo zithuzi zomwe ayimira limodzi pomwe amakalandilidwa pa bwalo la ndege ponthawi yomwe amafika mdziko la UK ndipo onse anali ali mwee, kumwetulira.

Anthu ena omwe ayikira ndemanga pa tsamba la fesibuku la Tay Grin yemwe dzina lake leni leni ndi Limbani Kalirani, ati aphunzira kuti nkhani za anthu omwe ali nchikondi sibwino kumalankhula kwambiri pakachitika chinthu.

“Lero limenelo? Ayi zikomo. Ife nde tinagundikatu kumunyoza mulamu pa Zambia, taphunzira ndipodi ndi zoona kuti nkhani za anthu omwe anaoneranapo osamalowelera,” watelo munthu wina poikira ndemanga zithunzi zomwe Tay Grin waika pa tsamba lake la fesibuku.

Nkhani yoti awiriwa agwa mchikondi inadziwika kwambiri mwezi wa November chaka chatha kamba ka zithuzi za chikondi zomwe awiriwa anazivumbwitsa m’masamba a nchezo awo ndipo akhala akuyendera limodzi kuona chilengedwe mdziko la Zambia komaso kuno ku Malawi.

Advertisement