Achinyama 4,000 amene anakonza ziphaso zawo ndi ndondomeko zonse kuyembekezera kunyamuka ulendo okagwira ntchito ku minda mdziko la Israel, ati lero akumana pa manda a Kamuzu pa ulendo wawo wokachita m’bindikiro ku ma ofesi aboma, kudandaulira ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna (OPC) mu Mzinda wa Lilongwe.
M’malingana ndi m’modzi mwa achinyamata omwe Malawi24 yayankhula nawo ku m’mawaku, omwe akutsogolera nawo m’bindikilowu a Samson Maganga, ati tsogolo lonyamuka layamba kuchita m’dima popeza palibe chomwe chikuchitika chowonetsa kunyamuka ulendo opita ku Israel ndipo ati nkhaniyi ikhonza kufera m’mazira.
A Maganga ati iwo monga guru lokhudzidwa alemba kale kalata kupita kwa mtsogoleri wa dziko kuwakumbutsa kuti achinyamatawa adatsata njira zonse zofunika zokhudza ulendo wa ku Israel komanso kuti boma lidatsimikiza kuti pofika pa 31 March, 2024 achinyamata akhala atanyamuka koma ati palibe chikuonetsa za ulendo.
“Ife palibenso komwe tingapite koma tupita kukadandaulira mtsogoleri wa dziko kuti akwanilitse khumbo lathu maka mogwilizananso ndi zomwe adalankhula mnyumba ya malamulo pamene adafunsidwa za ulendowu, ifeyo ngati achinyamata tonse okhudzidwa tilibe kwina kolowela tikakhala ku Capital Hill mpaka mayankho atapezeka” atelo a Maganga.
A Joyce Chitsulo omwe ndi wapampando wa aphungu owona za ubale wa Malawi ndi mayiko ena, masabata apitawo adati achinyamata okwana 2,500 akhala poyambila ndipo kuti khumbo la boma ndi kukwanitsa achinyamata 10, 000 omwe boma la Israel likufuna.
Achinyamatawa adadandaula kut zikalata zawo za chipatala zitha mphamvu zomwe ziwakakamize kuti adzawonongenso ndalama zina kupangila zikalata zina, ndipo ati a mkhalapakati (agents) oyendetsa za ulendo wawo wawatsimikizira kuti iwo ali okonzeka ndipo akungodikira boma limalizitse mkuvomeleza kuti iwo anyamuke.