Anthu ochita malonda ochokera kwa Chinseu m’dera la Zomba Lisanjala anachita m’bindikiro ku office ya Escom mu mzinda wa Zomba powonetsa mkwiyo wao kuti akhala miyezi isanu opanda magetsi potsatira kupsa kwa transformer mdelaro.
Poyankhula ndi Malawi24, m’modzi mwa anthu omwe akutsogolera pochita m’bindikirowo a Leonard Phiri ati cholinga chawo akufuna kuti bungwe la Escom likawayikire transformer kwa Chinseu chifukwa akhala masiku 150 yomwe ili miyezi isanu (5) opanda magetsi ndipo ntchito zamalonda zidayima.
A Phiri ati akhala akukambirana ndi akulu akulu a Bungwe la Escom kwa nthawi yayitali koma amangowalonjeza kuti awayikira transformer yatsopano koma tsopano atopa ndikudikira.
Iwo ati anthu ochita malonda monga zigayo, owotchelera zitsulo, ometa komanso ogulitsa zokumwa zinthu sizikuwayendera ndipo akugona ndi njala popeza sakugwira ntchito ina iliyonse akungokhala.
Iwo awopseza kuti akhalabe akuchita m’bindikirowo mpaka magetsi ayambirenso kuyaka mdera la Chinseu..
A Phiri adatinso mdera la Chinseu kulinso chipatala chomwe ndipo chinasiya kusunga mankhwala omwe amafunika kukhala mmalo ozizira.
Pamenepa iwo apempha bungwe la Escom komanso Boma kuti awayikire transformer yatsopano kuti ntchito zamalonda ziyambirenso kuyenda bwino.
“Ophunzira omwe akukonzekera kulemba mayenso akulephera kuwerenga chifukwa chosowa magetsi komanso amai omwe akufuna kuchira (kubereka) akapita kuchipatala akumavutika popeza kuchipatalako kulibe magetsi,” adadandaula motero a Leonard Phiri.
Koma Malawi24 itafuna kumva zankhaniyi kuchokera kwa Phungu wamdera la Zomba Lisanjala Dr William Susuwele Banda, iwo adati nkhani yakuvuta kwa magetsi kwa Chinseu akuyidziwa ndipo adati adakambirana kale ndi Bungwe la Escom ndipo adawalonjeza kuti awayikira transformer ikapezeka popeza madera omwe akusowekera ma transformer ndi ambiri.
Dr Susuwele Banda adati sakuwona chifukwa chochitira m’bindikiro ku ofesi ya Escom popedza nkhaniyi adayikambirana kale ndipo chomwe chatsala ndichoti kubwere transformer ina.